Sports Line Malawi

Your number one spot for Malawian aswell as international Sports. We cover Highlights, Reactions, Analysis, Local Talent and International Updates. Subscribe and stay in the game with Sports Line Malawi


Sports Line Malawi

#NKHANI

Elia Kananji wasayina mgwirizano wa miyezi isanu ndi timu ya Goshen City Dedza Dynamos, kuti atsogolere timuyi mpaka kumapeto kwa season ino.

Mkulu wa timuyi, a Hazwell Gamphani, watsimikiza za nkhaniyi.

Kananji walowa m'malo mwa Alex Ngwira, yemwe anachotsedwa ntchito ku timuyi.

Mphunzitsi watsopanoyu wayamba zokonzekera ndi timuyi m'mawa wa lero, pokonzekera masewero a Loweruka mu mpikisano wa FDH Bank Premiership ndi CIVO Service United pa bwalo la CIVO ku Lilongwe.

Source : #zbsnews

3 days ago | [YT] | 4

Sports Line Malawi

#Breaking news

Team ya Ekhaya fc yaimitsa ntchito mphunzitsi wawo wamkulu Enos chatama. izi zatsimikizika kudzera mu chikalata chomwe team yi yatilutsa.

1 month ago | [YT] | 11

Sports Line Malawi

MALAWI MALAWI 🔥

Team ya mpira wa myendo koma ya atsikana ya Scorchers yafika mu ndime yotsiliza (Finals) ya mpikisano wa Wafcon.

Team yi yagonjetsa Algeria ndi zigoli zitatu kwa chimodzi (3-1) zigoli zochokera kwa Tabitha komanso Temwa Chawinga.

Congratulations scorchers...titenge chinthuchi!!

#SLM

2 months ago | [YT] | 9

Sports Line Malawi

SCORCHERS SCORCHERS 🔥🔥🔥

Team ya mpira wa myendo koma wa atsikana ya dziko lino ya scorchers yagonjetsa team ya Ghana ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi .

Mmene zateromu malawi ikhale ikufika mu semi final ya mpikisano umenewu wa wafcon komanso yadzigulira malo ku mpikisano wa world cup omwe uchitike chaka cha mmawa ku Brazil.

Congratulations scorchers!!

2 months ago | [YT] | 13

Sports Line Malawi

#NKHANI

Team ya scorchers yapitilira mu ndime ya quarter final mu mpikisano wa wafcon omwe ukuchitikira ku morroco.

Scorchers yangonja ndi team ya zambia 2-1 koma zigoli ndi zomwe zapulumutsa team yi.

Congratulations scorchers!

2 months ago | [YT] | 4

Sports Line Malawi

#NKHANI

Team ya mpira wa myendo koma wa atsikana dziko muno ya scorchers, yagonjetsa Team ya Nigeria ndi zigoli zitatu(3) kwa ziwiri (2). Iyi inali game yoyamba ya scorchers mu mpikisano wa women's africa cup of nations (WAFCON) omwe ukuchitikira ku morroco.

Temwa chawinga wagoletsa zigoli ziwiri ndipo chinacho wagoletsa ndi Tabitha chawinga.

Scorchers ikhala ikukumana ndi egypt lowerukali mmasewero awo otsatira.

#SLM

2 months ago | [YT] | 10

Sports Line Malawi

#NKHANI

Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yatsimikiza kuti yasiyana ndi osewera pakati ku timuyi, Mike Mkwate.

Izi zachitika mbali zonse zitamvana posawonjezera mgwirizano watsopano.

Mkwate anayamba kutumikira timuyi m'chaka cha 2016, asanapite m'dziko la South Africa komwe anali mu timu ya Polokwane City m'chaka cha 2021.

Iye anabweleranso ku FCB Nyasa Big Bullets mu chaka cha 2023.

Pakadali pano Bullets yati ikufunira Mkwate zabwino komanso yamuthokoza pa nthawi yomwe katswiriyu watumikira timuyi.

Source:#mijonline

3 months ago | [YT] | 3

Sports Line Malawi

FULL TIME

Bullets 1-0 Masters FC

Ephraim Kondowe’s second-half penalty is enough to seal all three points as Maule record back-to-back league victories while extending the unbeaten start to the season.

3 months ago | [YT] | 2

Sports Line Malawi

The Super League of Malawi have announced that the FDH Bank Premiership match between FCB Nyasa Big Bullets and Masters on Saturday 27 June 2026 has been moved from Mpira Stadium to Joyce Chitsulo Stadium in Mwanza.

Additionally, the Silver Strikers and Red Lions match, which was scheduled for Saturday 27 June 2026, has been rescheduled to Sunday 28 June 2026.

These changes are due to unavailability of Mpira and Silver Stadium on the scheduled dates.

Please note that kick-off times for both fixtures remain unchanged.

3 months ago | [YT] | 0

Sports Line Malawi

#NKHANI

Katswiri watimu ya Denmark, Christian Eriksen, anagwa mmasewero omwe timuyi imakumana ndi Ukraine pokonzekera mpikisano wa FIFA World Cup.

Koma akuluakulu a timu yi akuti katswiriyu alibwinobwino ndipo anatuluka yekha koma pakadali pano apita naye ku chipatala kuti akamuyeze.

Aka ndi kachiwiri Eriksen kugwa mu bwalo la zamasewero. Timufunira kuchila mwansanga katswiriyu.

4 months ago | [YT] | 4