Genz Community


Zinsisi TV

"A Namalomba asanduka apolisi kapena iwo aja ndi a ACB?"- Suleman

Sipikala wa nyumba ya malamulo Sameer Suleman wati mneneri wa boma Shadric Namalomba alibe mphamvu zowauza kuti apeleke umboni pa katangale yemwe wakula m'boma.

Suleman walankhulapo, a Namalomba atapeleka masiku 7 kuti a Suleman awapatse umboni pa nkhani za katangale zomwe akunenazo.

Koma Suleman wati a Namalomba si wapolisi komanso sagwira ntchito ku bungwe la ACB kuti afune umboni.

Sipikalayu wauza a Namalomba kuti adutsa malire a ntchito yawo yongolankhulira boma kapena chipani.

Iwo atsindika kuti ali ndi umboni okwanira pa zomwe akunena ndipo ndi okonzeka kugwira ntchito ndi nthambi zoyenerera kuti chilungamo chioneke.

1 week ago | [YT] | 155

Zinsisi TV

R.I.P.
BRIAN BANDA 💔

2 months ago | [YT] | 81

Zinsisi TV

Chief Resident Magistrate Austin Banda wati Namiwa akuyankha mlandu owukira boma (treason) komanso kufalitsa uthenga wabodza omwe ndiopeleka mantha kwa anthu.

Bwalori lati Namiwa anayankhura pa kanema wa Luntha kuti ikamatha miyezi iwiri wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino Jane Ansah akhala mtsogoleri wadziko lino.

Malingana ndi mndandanda wamlanduwu, zomwe anayankhurazi ndizodabwitsa kaamba kakuti pampando wa mtsogoleri wadziko pali munthu kale.

Banda watumiza mlanduwu kubwalo lalikulu komwe likapitilire kumva kuonjezerapo pempho la belo.

2 months ago | [YT] | 20

Zinsisi TV

TIKUKUFUNILANI EID YOPAMBANA KWA ASILAMU NONSE OMWE MUMATSATILA ZINSISI TV YOUTUBE CHANNEL

ZIKOMO KWAMBIRI TIMAKUNYADILANI

7 months ago | [YT] | 13

Zinsisi TV

Akuluakulu abungwe la Malawi First ali ku maofesi a bungwe lolimbana ndi katangale ndi ziphuphu komwe mwazina akuti akufuna akupereka kalata ya umboni okhudza kukula kwa mchitidwe wa katangale omwe akuganiza kuti ukuchitika ku Reserve Bank of Malawi (RBM).

Iwo akuti katangaleyu wakula pakayendetsedwe ka ndalama za mthumba la anthu opuma pa ntchito (Pensions Fund).

Koma, patha maola angapo tsopano akuluakulu a bungwe la ACB asanatuluke ndipo achitetezo atseka chipata cholewera kumaofesiwa achitseka.

8 months ago | [YT] | 28

Zinsisi TV

Sipikala wa nyumba ya Malamulo Sammier Suleman wauza aphungu akuti munthu wina yemwe sakudziwika wagwetsa chithumwa,pafupi ndi chipata chomwe aphungu amalowera nyumbayi.

Ndipo iye wapempha yemwe wagwetsa chinthuchi kuti apite akatole chifukwa anthu ogwiri tchito ku nyumba malamulo akuchita nacho mantha

Suleman wati amene wagwetsa asadzayambireso chifukwa anthu ena mnyumbayi amakhulipilira mulungu.

"Zimenezi musamalowe nazo myumba muno,muzidzisiya kunyumba" Suleman anatero

8 months ago | [YT] | 20

Zinsisi TV

Amene adali mkulu wa bungwe la Neef a Humphrey Mdyetseni komanso mmodzi wa akuluakulu aku nthambi ya ulimi wamthirira pansi pa unduna wa za ulimi a Anderson Mbozi afika ku bwalo la milandu mu mzinda wa Lilongwe.

M'bwaloli, awiririwa akuyembekezeka kuwauza milandu imene apolisi awamangira.

Apolisi adamanga awiriwa masiku apitawa powaganizira milandu yokhudza kugwiritsa ntchito udindo wawo molakwika.

8 months ago | [YT] | 11

Zinsisi TV

Mmodzi wa anthu odziwika bwino mmasamba a mchezo VJ Ken wanjatidwa kaamba komuganizira kuti amasunga mokakamiza mwana wa zaka khumi ndi zisanu 15 komanso kupanga naye ubwenzi.

Apolisi a Ndirande ku Blantyre ndi omwe amanga mkuluyu yemwe dzina lake lenileni ndi Kenneth Makina.

Malinga ndi mneneri wa polisi ya Ndirande a Chibisa Mulimbika, atamufunsa za izi VJ Ken anavomera kuti anali pa ubwenzi ndi mwanayu koma samadziwa kuti ndi wachichepere.

A Mulimbika ati mwanayu anavomeranso kuti ndi VJ Ken anali pa ubwenzi womachita zogonana.

Woganiziridwayu akuyembekezeka kuonekera ku bwalo la milandu lero kuti akayambe kuyankha milandu iwiriyi.

VJ Ken yemwe alinso ndi luso lojambula makanema amachokera mmudzi wa Ndelema mfumu yaikulu Symon m'boma la Neno.

11 months ago | [YT] | 34

Zinsisi TV

Tachipatseni dzina labwino chigalimo ichi

11 months ago | [YT] | 34

Zinsisi TV

Unduna owona zokopa alendo wasankha Rashley kuti ayimbe nyimbo ya mwezi olimbikitsa ntchito zokopa alendo, umene umayamba pa 1 mpaka pa 31 September.

Poyankhula nafe madzulowa, nduna mu undunawu a Vera Kamtukule yati undunawu wasankha Rashley kamba kakuti ndi woyimba waluso lapamwamba amene akhoza kugwira ntchitoyi mwa ukadaulo.

Iwo ati, alandira thandizo la 1 million kwacha kwa achifundo ena (donor) yogwilira ntchitoyi.

Nkhaniyi yadza pamene Rashley anapepesa kwa a Malawi posachedwa kamba ka zina zomwe sanachite bwino m'mbuyomu, ndipo wati akufuna kuti luso lake loyimba liyambenso kuyenda bwino ngati kale.

Ndipo zinthu zikuwoneka kuti zayamba kusonya tsopano kwa Rashley, pomwe lero a UMP Festival alengezanso kuti woyimbayu akakhala nawo kuphwandoli ku Mangochi.

(by Innocent Kumchedwa - Lilongwe;08/27/25)

#malawismostfollowedpage

1 year ago | [YT] | 53